Psalms 32

Salimo la Davide. Malangizo.

1Ngodala munthu
amene zolakwa zake zakhululukidwa;
amene machimo ake aphimbidwa.
2Ngodala munthu
amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.

3Pamene ndinali chete,
mafupa anga anakalamba
chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
4Pakuti usana ndi usiku
dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
monga nthawi yotentha yachilimwe.
Sela
5Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
mlandu wa machimo anga.”
Sela

6Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
sadzamupeza.
7Inu ndi malo anga obisala;
muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
ndi nyimbo zachipulumutso.
Sela

8Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
9Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
koma chikondi chosatha cha Yehova
chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.

11Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
Copyright information for NyaCCL